Mawu A Mulungu A Chipangano Chatsopano : Gods Word, The New Testament (Chichewa) Trinitarian Bible Society 2024
This is the Chichewa language translation of the New Testament. Chichewa is spoken in Malawi (particularly the northern part), and southern Zambia, and a small part of Zimbabwe. This is a translation into Chichewa of the traditional Received Text, by the Trinitarian Bible Society (TBS).
Size: A5 format: 202mm x 141mm, 21mm thick ( 400 g )
Pages: 416 pages
Text size: 9 pt font size, 12 pt line spacing
Format: One column
Cover: Hard cover, Navy blue
Text Copyright: ©2024 Trinitarian Bible Society
Contents: Mateyu, Mariko, Luka, Yohane, Machitidwe, Aroma, 1 Akorinto, 2 Akorinto, Agalatiya, Aefeso, Afilipi, Akolose, 1 Atesalonika, 2 Atesalonika, 1 Timoteyo, 2 Timoteyo, Tito, Filemoni, Ahebri, Yakobo, 1 Petro, 2 Petro, 1 Yohane, 2 Yohane, 3 Yohane, Yuda, Chivumbulutso
Text sample (part of John 1):
1 Mu chiyambi munali Mawu, ndipo Mawu adali ndi Mulungu, ndipo Mawu adali Mulungu.
2 Omwewa adali mu chiyambi ndi Mulungu.
3 Zinthu zonse zidapangidwa ndi iye; ndipo popanda iye sikadalengedwe kanthu kena kalikonse kamene kadalengedwa.
4 Mwa iye mudali moyo; ndi moyowu udali kuwunika kwa anthu.
5 Ndipo kuwunikaku kuwala mu mdima; ndi mdimawu siudakuzindikira ayi.
6 Padali munthu, wotumidwa kuchokera kwa Mulungu, amene dzina lake [lidali] Yohane.
7 Yemweyu adadza chifukwa cha umboni, kudzachita umboni za Kuwunika kumeneko, kuti [anthu] onse kudzera mwa iye akhoze kukhulupirira.
8 Iye sianali Kuwunika kumeneku, koma [adatumidwa] kukachita umboni wa Kuwunika kumeneku.
9 [Kumeneko] kunali Kuwunika kwenikweni, kumene kuwunikira munthu aliyense amene adza kulowa mdziko lapansi.
10 Iye adali mdziko lapansi, ndipo dziko lapansi lidalengedwa ndi iye, ndipo dziko lapansi silidamdziwe iye.
11 Anadza kwa ake a iye yekha, ndipo ake a mwini yekha siadamlandire iye.
12 Koma ambiri iwo amene anamlandira iye, kwa iwo iye adapatsa mphamvu kuti akhale ana amuna a Mulungu, [ngakhale] kwa iwotu amene akhulupirira dzina lake.
13 Amene anabadwa, osati mwa mwazi, kapena mwa chifuniro cha thupi, kapena ndi chifuniro cha munthu, koma cha Mulungu.
14 Ndipo Mawu adasandulika thupi, nakhazikika pakati pa ife, (ndipo ife tidawona ulemerero wake, ulemerero wonga wa wobadwa yekha wa Atate), wodzala ndi chisomo ndi chowonadi.
15 Yohane achita umboni za iye, ndipo anafuwula, kunena kuti, Uyu ndi iye amene ine ndidanena za iye, Iye wakudzayo pambuyo panga adalipo ndisanabadwe ine: pakuti adali woyamba wa ine.
16 Ndipo mwa kudzala kwake ife tonse talandira, chisomo kwa chisomo.
17 Pakuti chilamulo chidapatsidwa mwa Mose, [koma] chisomo ndi chowonadi zinadza mwa Yesu Khristu.
18 Palibe munthu adawona Mulungu nthawi ina iliyonse; Mwana wamwamuna wobadwa yekha, amene ali mchifukato cha Atate, iyeyu walengeza [iye].
...